Deuteronomy 12:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzikapereka nsembezo pa malo amodzi okha, amene Chauta adzasankhule pakati pa mafuko anu. Muzikapereka nsembe zanu zopsereza pa malo okhawo, ndipo kumenekonso muzikachita zina zonse zimene ndikukulamulani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mafuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzichita zonse ndikuuzani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukaphere pa malo okhawo amene Yehova adzawasankhe mwa limodzi la mafuko anu, ndipo kumeneko mukasunge chilichonse chimene ndikulamulireni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mapfuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzicita zonse ndikuuzani.