Deuteronomy 12:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku midzi yonse kumene mukakhale, mungathe kumakaphako zoŵeta zanu kuti muzikadya. Muzidzadya monga mungafunire, malinga nchifundo cha Chauta, Mulungu wanu, chimene Iye wakupatsani. Nonsenu muzikadya, amene ali oipitsidwa pa zachipembedzo ndi amene ali osaipitsidwa. Monga momwe mukadadyera nyama yamphoyo kapena yangondo, muzikachita chimodzimodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma monga mwa chikhumbu chonse cha moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m'midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mukhoza kumapha ziweto zanu mʼmizinda iliyonse ndi kudya nyama yake mmene mungafunire, ngati kuti ndi agwape kapena mbawala, monga mwadalitso limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Woyeretsedwa ndi wosayeretsedwa akhoza kuyidya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma monga mwa cikhumbu conse ca moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m'midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo.