Deuteronomy 12:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inuyo ndi ana anu, pamodzi ndi antchito anu, ndi Alevi amene akhala m'midzi mwanu, muzikadya zopereka zonsezi pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atasankha. Kumenekonso muzidzasangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha ntchito zanu zonse zoyenda bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mʼmalo mwake, muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhira inu, ana anu aamuna ndi aakazi, antchito anu aamuna ndi adzakazi anu, ndi Alevi ochokera mʼmizinda yanu, ndipo mudzasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa chilichonse chimene mudzachikhudza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.