Deuteronomy 12:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mutalanda maiko a anthuwo, musadzalephere kuwononga kwathunthu malo onse amene iwo amapembedzerapo milungu yao, monga pa mapiri aatali ndi pa mapiri aafupi, ndiponso pansi pa mitengo yogudira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri aatali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muwonongeretu kwathunthu malo onse a pamwamba pa mapiri ataliatali ndi pa mapiri angʼonoangʼono ndi pansi pa mtengo uliwonse wotambalala pamene mitundu imene muyilande dzikolo ankapembedzerapo milungu yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri atali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;