Deuteronomy 12:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wanu, akadzalikuza dziko lanulo monga momwe adakulonjezerani, pamene mudzamva nkhuli, mudzatha kukhuta nyama monga momwe mudzafunire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wanu akadzakulitsa dziko lanu monga anakulonjezerani, ndipo mukapukwa nyama mumanena kuti, “Ndikufuna nyama,” pamenepo mudzadya mmene mungafunire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.