Deuteronomy 12:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati ali patali malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankha kuti anthu azilemekezerako dzina lake, mungathe kupha ng'ombe yanu iliyonse kapena choŵeta china, monga ndidakuuzirani. Muphe nyama mwa zimene Chauta akupatsani, ndipo mudye nyama kwanu, monga momwe mungafunire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lake akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati malo amene Yehova Mulungu wanu awasankha kuti ayike Dzina lake ali kutali kwambiri ndi inu, mukhoza kupha ziweto pakati pa ngʼombe ndi nkhosa zimene Yehova wakupatsani, monga ndinakulamulani, ndipo mʼmizinda yanuyanu mukhoza kuzidya mmene mungafunire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lace akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.