Deuteronomy 12:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko mukapereke nsembe zopsereza, nyama ndi magazi omwe, pa guwa la Chauta. Magazi ake mukathire pa guwa la Chauta, Mulungu wanu, koma nyama yake mungathe kudya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yake muidye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mupereke nsembe zanu zopsereza pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, nyama pamodzi ndi magazi omwe. Magazi a nsembe zanu athiridwe pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyamayo mukhoza kudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yace muidye.