Deuteronomy 12:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukagwetse maguwa ao, ndipo miyala yao yoimiritsa, imene amaiyesa yopembedzerapo, mukaiphwanyephwanye. Mukatenthe mafano ao a Aserimu. Mukaonongenso mafano ao ofanizira milungu yao, ndipo mukafafanize ndi dzina lomwe la milunguyo konsekonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao lichoke m'malomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mugumule maguwa awo ansembe, ndi kuphwanya miyala yawo yachipembedzo ndipo mutenthe pa moto mafano awo a Asera: mugwetse mafano a milungu yawo ndi kufafaniza mayina awo mʼmalo amenewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao licoke m'malomo.