Deuteronomy 12:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musadzapembedze Chauta, Mulungu wanu, mofanafana ndi m'mene iwo amapembedzera milungu yaoyo. Iwo adachita zoipa zoopsa zambiri zimene Chauta amadana nazo, mpaka kutentha ana ao aamuna ndi aakazi pa moto pakuŵapereka kwa milungu yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musapembedze Yehova Mulungu wanu momwe amachitira iwowo, chifukwa popembedza milungu yawoyo amachita zonyansa zamitundumitundu zimene Yehova amadana nazo. Amatentha ngakhale ana awo aamuna ndi aakazi pa moto ngati nsembe za kwa milungu yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti ziri zonse zinyansira Yehova, zimene azida iye, iwowa anazicitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.