Deuteronomy 12:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adzasankha malo amodzi m'dziko mwanu, ndipo anthu onse azidzabwera kudzampembedza pa malo amenewo. Kumeneko ndiko kumene mudzapite.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu muzifunafuna kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati pa mafuko anu kuti ayikeko dzina lake ndi kukhalako. Ku malo amenewa muyenera kupitako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mapfuko anu onse kuikapo dzina lace, ndiko ku cokhalamo cace, muzifunako, ndi kufikako;