Deuteronomy 12:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumenekonso inu pamodzi ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha madalitso amene Iyeyo adatsitsa pa inu, kuti ntchito zanu zonse ziyende bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo kumeneko muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m'mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko, pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalalako pa china chilichonse chimene mudzakhudza, chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo kumeneko muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m'mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani.