Deuteronomy 13:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumuphe ndi miyala. Iye adati akusokeretseni, kuti musiyane ndi Mulungu wanu amene adakutulutsani ku dziko la Ejipito kumene mudaali kuukapolo kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukuchetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya akapolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumuponye miyala mpaka kumupha, chifukwa anafuna kukupatutsani pa njira ya Yehova Mulungu amene anakutulutsani ku Igupto, dziko la ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukucetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba va akapolo.