Deuteronomy 13:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zinthu zonse za anthu a mu mzinda umenewo muzisonkhanitse pamodzi, ndipo muziwunjike pakati pa bwalo lalikulu la mzindawo. Tsono mutatero, muutenthe mzindawo pamodzi ndi zonse zam'menemo, kuti zikhale ngati nsembe yopsereza kwa Chauta, Mulungu wanu. Muusiye choncho kuti ukhale bwinja mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muzikundika zofunkha zake zonse pakati pakhwalala pake, nimutenthe ndi moto mudzi, ndi zofunkha zake zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Katundu yense wa anthu mu mzindawo mumuwunjike pamodzi pakatikati pa bwalo losonkhanako ndipo mutenthe mzindawo pamodzi ndi katundu wake yense monga nsembe yathunthu yopsereza ya kwa Yehova Mulungu wanu. Mzinda umenewo ukhale bwinja mpaka muyaya, usadzamangidwenso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muzikundika zofunkha zace zonse pakati pakhwalala pace, nimutenthe ndi moto mudzi, ndi zofunkha zace zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.