Deuteronomy 13:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musagwireko kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono Chauta adzaleka osakukwiyiraninso, adzakumverani chisoni ndipo adzakuchitirani chifundo, nadzakuchulukitsani monga adalonjezera makolo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musapezeke ndi kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa kuti Yehova abweze mkwiyo wake wochititsa manthawu. Adzakuchitirani chifundo ndi kukumverani chisoni, ndipo adzakuchulukitsani monga analonjeza mwa lumbiro kwa makolo anu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka cinthu coti cionongeke; kuti Yehova a aleke mkwiyo wacewaukali, nakucitireni cifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukucurukitsani monga analumbirira makolo anu;