Deuteronomy 13:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma aphedwe mneneri aliyense kapena womasulira maloto aliyense amene akuuzani kuti muukire Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito ndi kukuwombolani m'dziko laukapolo. Munthu wotero ndi woipa, chifukwa akufuna kukusiyitsani njira imene Chauta akufuna kuti muitsate. Aphedwe, ndipo pakutero mudzachotsa choipa chimenechi pakati panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, nakuombolani m'nyumba ya akapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mneneri kapena wolotayo ayenera kuphedwa, popeza analalikira zopandukira Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo. Wolalikirayo anafuna kukupatutsani pa njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani kuti muyitsatire. Muzichotsa choyipa pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena cosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, nakuombolani m'nyumba ya akapolo; kuti akuceteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzicotsa coipaco pakati pa inu.