Deuteronomy 13:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu atha kukunyengererani mobisa kuti mupembedze milungu ina, milungu imene inu ndi makolo anu simudaipembedzepo. Munthuyo ngakhale akhale mbale wanu weniweni wa mimba imodzi kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena bwenzi lanu lapamtima, musaipembedze milunguyo mpang'ono pomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwa, inu, kapena makolo anu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mʼbale wanu weniweni kapena mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena mnzanu wapamtima akukakamizani mwachinsinsi, nʼkumati, “Tiyeni tipite tikapembedze milungu ina” (milungu imene inuyo kapena makolo anu sanayidziwe,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanu wanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu yina, imene simunaidziwa, inu, kapena makolo anu;