Deuteronomy 14:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndinu ake a Chauta, Mulungu wanu, popeza kuti wakusankhulani pakati pa anthu a pa dziko lonse lapansi, kuti mukhale anthu akeake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu. Pakati pa anthu onse pa dziko lonse lapansi, Yehova wasankha inu kuti chikhale chuma chake chamtengo wapatali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope pa dziko lapansi.