Deuteronomy 14:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mwina mtunda udzakutalikirani chifukwa kwatalikitsa kumalo kumene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azimpembedzerako. Motero inu mudzalephera kupita nawo kumeneko magawo anu achachikhumiwo, amene mwaŵapeza chifukwa cha madalitso a Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lake, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati malo amenewa ali kutali kwambiri ndipo kuti inu mwadalitsidwa ndi Yehova Mulungu wanu, ndipo simungathe kunyamula chakhumi chanu (chifukwa chakuti malo amene Yehova adzasankha kukayikako dzina lake ali kutali kwambiri),
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lace, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;