Deuteronomy 14:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndalamazo mugulire zilizonse zimene mufuna, monga nyama yang'ombe, nyama yankhosa, vinyo ndiponso zakumwa zaukali, malinga nkukhosi kwanu. Tsono inuyo pamodzi ndi mabanja anu, mudzadye ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mugule ndi ndalamazo chilichonse moyo wanu ukhumba, ng'ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena chakumwa cholimba, kapena chilichonse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gwiritsani ntchito silivayo kugula chilichonse chimene muchifuna monga ngʼombe, nkhosa, vinyo kapena zakumwa zina zosasitsa, kapena china chilichonse chimene muchifuna. Ndipo inu ndi anthu a pa banja panu mudzazidyera komweko pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kukondwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mugule ndi ndaramazo ciri conse moyo wanu ukhumba, ng'ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena cakumwa colimba, kapena ciri conse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu.