Deuteronomy 14:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Alevi amene mumakhala nawo m'midzi mwanu musaŵaiwale, popeza kuti alibe dziko kapena choloŵa chaochao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi okhala mʼmizinda yanu musaleke kuwathandiza popeza alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu.