Deuteronomy 14:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chakudya chimenechi ncha Alevi, poti alibe zaozao. Ndiponso ncha alendo ndi cha ana amasiye ndi akazi amasiye amene amakhala nanu pamodzi m'midzi mwanu. Anthu otere azibwera kudzatenga zimene akusoŵa. Muzichita zimenezi kuti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitseni pa ntchito zanu zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu ntchito zonse za dzanja lanu muzichitazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu nchito zonse za dzanja lanu muzicitazi.