Deuteronomy 14:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pakati pa nyama zaziboda kapena zobzikula, musadye izi: ngamira, kalulu ndi mbira, chifukwa ngakhale zimabzikula, koma zilibe ziboda zogaŵikana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda: ngamira, ndi kalulu, ndi mbira, popeza zibzikula, koma zosagawanika chiboda, muziyese zodetsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe pakati pa nyama zimene zimabzikula kapena zogawikana zipondero, zimene simukuyenera kudya ndi ngamira, kalulu ndi mbira. Zimenezi ngakhale zimabzikula, zipondero zake sizogawikana, choncho ndi zodetsedwa, musadye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika ciboda: ngamila, ndi ka'ulu, ndi mbira, popezazibzikula, komazosagawanika ciboda, muziyese zodetsa;