Deuteronomy 15:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzampatseni mwaufulu mosaŵinya, ndipo Chauta adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumupatse iye mowolowamanja ndipo muchite zimenezi mosasungira kanthu kumtima. Tsono chifukwa cha zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse ndi pa chilichonse chimene mukhudza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, cifukwa ca ici Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu nchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu.