Deuteronomy 15:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi zonse padzakhala Aisraele ena osauka, osoŵa zinthu. Motero ndikukulamulani kuti otereŵa muzidzaŵachitira chifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu osauka sadzatha mʼdziko lanu. Chomwecho ndikukulamulani kuti mukhale ofewa manja kwa abale anu ndi kwa osauka, osowa mʼdziko mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza waumphawi salekana m'dziko, cifukwa cace ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.