Deuteronomy 15:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muhebri mnzanu, mwamuna kapena mkazi, akadzigulitsa kwa inu kuti akhale kapolo wanu, mummasule atangokutumikirani zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, mumlole kuti apite mwaufulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukagula mbale wanu, Muhebri wamwamuna kapena Muhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi chimodzi; koma chaka chachisanu ndi chiwiri umlole achoke kwanu waufulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mʼbale wanu wamwamuna kapena wamkazi adzigulitsa yekha kwa inu, nakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, muzimumasula mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukagula mbale wanu, Mhebri wamwamuna kapena Mhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi cimodzi; koma caka cacisanu ndi ciwiri umlole acoke kwanu waufulu.