Deuteronomy 15:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumasula kapolo, kuti akhale mfulu, kusakuipireni. Adakutumikirani kale zaka zisanu ndi chimodzi pa theka la mtengo wa wantchito wolembedwa. Chitani zimenezi, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamayesa nchosautsa, pomlola akuchokereni waufulu; popeza anakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi monga wolipidwa wakulandira chowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musaone ngati chopweteka kumasula wantchito wanu, chifukwa ntchito imene wayigwira pa zaka zisanu ndi chimodzi zimenezi ndi yopindula kawiri pa ntchito imene akanagwira waganyu chabe. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamayesa neosautsa, pomlola akucokereni waufulu; popeza anakugwirirani nchito zaka zisanu ndi cimodzi monga wolipidwa wakulandira cowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzicita.