Deuteronomy 15:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana onse amphongo oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a zoŵeta zina, muŵapatule kuti akhale a Chauta, Mulungu wanu. Ng'ombe zimenezi musazigwiritse ntchito, ndipo nkhosazo musazimete bweya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa ntchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumupatulire Yehova Mulungu wanu choyamba kubadwa chachimuna chilichonse pa ngʼombe ndi nkhosa zanu. Musamazigwiritse ntchito ngʼombe zoyamba kubadwa kapena kumeta nkhosa zoyamba kubadwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa nchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.