Deuteronomy 15:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati pali kanthu kolakwika pa nyamayo, monga kutsimphina kapena khungu, kapena chilema chilichonse, musaphere nsembe Chauta nyama yoteroyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati chiweto chili ndi chilema monga kulumala kapena chosaona, kapena ngati chili ndi cholakwika chachikulu chilichonse, musachipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ikakhala naco cirema, yotsimphina, kapena yakhungu, cirema ciri conse coipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.