Deuteronomy 15:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mtundu wanu amene adzasauke, (poti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko limene Iye adzakupatsani ngati choloŵa chanu,)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe pasadzakhale wosauka pakati panu chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani kwambiri mʼdziko limene adzakupatsani kuti likhale lanu ngati cholowa chanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu canu;