Deuteronomy 15:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musadzakhale ndi maganizo achabe akuti, “Chaka chofafaniza ngongole chili pafupi.” Mukapanda kumuwonetsa mtima wachifundo mbale wanu wosaukayo, osampatsa kanthu, iyeyo adzakunenezani kwa Chauta molira, ndipo mudzapezeka olakwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dzichenjerani, mungakhale mau opanda pake mumtima mwanu, ndi kuti, Chayandika chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka cha chilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale tchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musayesere ndi pangʼono pomwe kusunga maganizo oyipa awa mu mtima mwanu: “Chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka chokhululukirana ngongole, chayandikira,” kuti musaonetse mtima woyipa kwa mʼbale wanu wosauka nʼkusamupatsa chilichonse. Iye angadzakunenereni inu mlandu kwa Ambuye, ndipo mudzapezeka wochimwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dzicenjerani, mungakhale mau opanda pace mumtima mwanu, ndi kuti, Cayandika caka cacisanu ndi ciwiri, caka ca cilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale cimo.