Deuteronomy 16:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukhale okondwa pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wamu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu pamodzi m'mizinda mwanu. Zimenezi muzichitira pa malo opembedzerapo aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi a mʼmizinda mwanu, alendo, ana ndi akazi amasiye okhala pakati panu, mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku malo amene adzawasankhe kukhazikitsako dzina lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace.