Deuteronomy 16:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musangalale pa chikondwererocho, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wanu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu m'mizinda mwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nimukondwere m'madyerero mwanu, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye okhala m'mudzi mwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musangalale pa chikondwerero chanu, inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi, alendo, ana ndi akazi amasiye amene ali mʼmizinda yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nimukondwere m'madyerero mwanu, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye okhala m'mudzi mwanu.