Deuteronomy 16:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzidzatamanda Chauta, Mulungu wanu, pochita chikondwerero chimenechi masiku asanu ndi aŵiri, pa malo amene Iye adzasankhule, chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atadalitsa kholola lanu ndi ntchito zanu zonse, kuti chimwemwe chanu chikhale chodzaza ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku asanu ndi awiri muchitire Yehova Mulungu wanu madyerero m'malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zipatso zanu zonse, ndi m'ntchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa masiku asanu ndi awiri muzichita chikondwererochi kwa Yehova Mulungu wanu kumalo kumene Yehova adzasankhe. Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani inu pa zokolola zanu ndi pa ntchito za manja anu, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku asanu ndi awiri mucitire Yehova Mulungu wanu madyerero m'malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zipatso zanu zonse, ndi m'nchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.