Deuteronomy 16:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'fuko lililonse mudzasankhe anthu oweruza ndiponso akuluakulu ena mu mzinda uliwonse umene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatseni. Anthu ameneŵa azidzaweruza anzao mosakondera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musankhe oweruza ndi akuluakulu a fuko lanu lililonse mu mzinda uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo adzaweruza anthuwa mwachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudziikire oweruza ndi akapitao m'inidzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mapfuko anu; ndipo aweruze anthu ndi ciweruzo colungama.