Deuteronomy 16:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asadzachite zinthu mopanda chilungamo kapena kuweruza milandu mokondera. Asadzalandire chiphuphu, chifukwa ziphuphu zimadetsa m'maso ngakhale anthu anzeru ndipo zimalakwitsa anthu olungama poweruza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, nichiipsa mau a olungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamapotoza ciweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira cokometsera mlandu; popeza cokometsera mlandu cidetsa maso a anzeru, niciipsa mau a olungama.