Deuteronomy 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyama ya nsembeyo musadye ndi buledi wotupitsa. Pa masiku asanu ndi aŵiri, muzidya nyamayo ndi buledi wosatupitsa ndiye kuti buledi wamazunzo, pakuti mudatuluka ku Ejipito mothaŵa. Motero masiku onse a moyo wanu, mudzakumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m'dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m'dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musadyere pamodzi ndi buledi wopanga ndi yisiti, koma kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti, buledi wa masautso, chifukwa munachoka ku Igupto mwamsangamsanga kuti pa masiku onse a moyo wanu muzikumbukira nthawi imene munanyamukira ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamadyera nayo mkaye wa cotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda cotupitsa, ndiwo mkate wa cizunziko popeza munaturuka m'dziko la Aigupto mofulumira; kuti inu kumbukile tsiku loturuka inu m'dziko la Aigupto masiku onse a moyo wanu.