Deuteronomy 16:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku asanu ndi aŵiri munthu wina aliyense asadzasunge chofufumitsira buledi m'nyumba mwake m'dziko mwanumo. Nyama imene idaphedwa madzulo pa tsiku loyamba, muzidzaidya kusanache.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'malire mwanu monse musaoneke chotupitsa masiku asanu ndi awiri; nyama yomwe muiphere nsembe tsiku loyamba madzulo, isatsaleko usiku wonse kufikira m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'malire mwanu monse musaoneke cotupitsa masiku asanu ndi awiri; nyama yomwe muiphere nsembe tsiku loyamba madzulo, isatsaleko usiku wonse kufikira m'mawa.