Deuteronomy 16:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muziphera pa malo amodzi opembedzerapo aja. Muzichita zimenezi poloŵa dzuŵa, ndiye kuti nthaŵi yomwe ija imene mudachoka ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma pamalo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsapo dzina lake, pamenepo muphere nsembe ya Paska, madzulo, polowa dzuwa, nyengo ya kutuluka inu m'Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma ku malo wokhawo amene Iye adzawasankhe kukhazikitsako Dzina lake. Kumeneko ndiye muzikapereka nsembe ya Paska madzulo, pamene dzuwa likulowa, pa tsiku lokumbukira kutuluka mu Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma pamalo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsapo dzina lace, pamenepo muphere nsembe ya Paskha, madzulo, polowa dzuwa, nyengo ya kuturuka inu m'Aigupto.