Deuteronomy 16:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wosatupitsa. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, muzisonkhana kuti mupembedze Chauta, Mulungu wanu, ndipo musadzagwire ntchito pa tsiku limenelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda chotupitsa; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira ntchito pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wopanda yisiti ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wa Yehova Mulungu wanu ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda cotupitsa; ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira nchito pamenepo.