Deuteronomy 17:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musadzapereke ng'ombe kapena nkhosa yachilema ngati nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu. Musadzapereke nyama iliyonse yopunduka, chifukwa Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala nacho chilema, kapena chilichonse choipa; pakuti chinyansira Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena cholakwika chilichonse, pakuti zimenezi zimamunyansa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala naco cirema, kapena ciri conse coipa; pakuti cinyansira Yehova Mulungu wanu.