Deuteronomy 17:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mutaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsenilo, ndipo mukadzafuna kuti mukhale ndi mfumu monga ili nayo mitundu ina yozungulira,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanulanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge, ndipo mukakakhazikika mʼmenemo nimunena kuti, “Tiyeni tisankhe mfumu yoti izitilamulira monga imachitira mitundu yonse yotizungulirayi,”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanu lanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga;