Deuteronomy 17:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumuyo isadzakhale ndi akavalo ambiri ndipo isadzatume anthu ku Ejipito kukagula akavalo, popeza kuti Chauta adakuuzani kuti, “Musadzabwererenso kumeneko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu mfumuyo isadzikundikire akavalo, kapena kutuma anthu kupita ku Igupto kukayipezera akavalo ena, pakuti Ambuye akuti, “Simuyenera kubweranso ku Igupto mʼnjira yomweyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma asadzicurukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu amke ku Aigupto, kuti acurukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.