Deuteronomy 17:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi zidzamthandiza kudziŵa kuti iyeyo saposa Aisraele anzake, ndiponso kuti sayenera kukhala wonyozera malamulo a Chauta mpang'ono pomwe. Motero iyeyo, pamodzi ndi zidzukulu zake zomwe, adzalamulira nthaŵi yaitali mu Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti achuluke masiku ake, m'ufumu wake, iye ndi ana ake pakati pa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asadzione kuti iyeyo ndi wopambana kuposa abale ake, nalekeratu kutsatira malamulo. Akasamala zimenezi iye ndi ana ake adzalamulira ufumu wa Israeli kwa nthawi yayitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti mtima wace usadzikuze pa abaleace, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti acuruke masiku ace, m'ufumu wace, iye ndi ana ace pakati pa Israyeli.