Deuteronomy 17:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Milandu yophana, yolimbirana zinthu, kapena yopwetekana m'mizinda mwanu, ikaŵavuta aweruzi anu, mupite ku malo achipembedzo aja osankhidwa ndi Chauta, Mulungu wanu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ukakukanikani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo milandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kunka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati akubweretserani milandu mʼmabwalo anu imene ili yovuta kuweruza kaya ndi yokhetsa magazi, kaya ndi yophwanyirana ufulu, kaya ndi yovulazana, muyitengere kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ukakulakani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo mirandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kumka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;