Deuteronomy 18:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe Achilevi, ndiye kuti fuko lonse la Alevi, asalandireko gawo m'dziko la Israele ngati choloŵa chao. Iwoŵa azidya zoperekedwa nsembe kwa Chauta ndi zina zoyenera Iyeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ansembe Alevi, fuko lonse la Levi, alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi Israele; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi cholowa chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe Achilevi amene ndi fuko lonse la Alevi, asapatsidwe malo kapena cholowa pakati pa Aisraeli. Iwowa azidzadya zoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe, popeza zimenezo ndiye cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ansembe Alevi, pfuko lonse la Levi, alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi Israyeli; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi colowa cace,