Deuteronomy 18:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakati panu pasadzapezeke wopereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto ngati nsembe. Pasaoneke munthu woombeza kapena woyeseza kulosa zam'tsogolo, kapena wogwiritsa ntchito nyanga kapena zithumwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pasapezeke pakati panu munthu wootcha pa moto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe. Asapezekenso pakati panu munthu wowombeza kapena wochita mawula, wolosera, wochita za ufiti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wace wamwamuna kapena mwana wace wamkazi ku mota wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.