Deuteronomy 18:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene mukukaŵalanda dziko limene mukakhalemolo, amatsata ndi kumvera amatsenga ndi oombeza. Koma inuyo Chauta, Mulungu wanu, sakulolani kuchita zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitundu ya anthu imene mudzayipirikitseyo imamvera anyanga kapena owombeza mawula. Koma inu Yehova Mulungu wanu sanakuvomerezeni kutero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kucita cotero.