Deuteronomy 18:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lija mudaasonkhana pa phiri la Horebuli, mudaapempha kuti, “Tisamvenso Chauta, Mulungu wathu, akulankhula, ngakhale kuwonanso moto waukulu choterewu, kuti tingafe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu m'Horebu, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuti tingafe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti izi ndi zimene munapempha kwa Yehova Mulungu wanu ku Horebu pa tsiku la msonkhano lija pamene munati, “Ife tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu kapena kuona moto woopsawu, kuopa kuti tingafe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu m'Horebe, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso mota waukuru uwu, kuti tingafe.