Deuteronomy 18:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mneneri wina aliyense woyerekeza kulankhula m'dzina langa, Ine osamulamula kuti atero, aphedwe. Ndipo ayeneranso kuphedwa mneneri wina aliyense wolankhula m'dzina la milungu ina.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m'dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mneneri wonena zinthu mʼdzina langa ndisanamulamulire kutero, kapena mneneri wonenera mʼdzina la milungu ina, ayenera kuphedwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mneneri wakucita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m'dzina la milungu yina, mneneri ameneyo afe.