Deuteronomy 18:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akati akulankhula m'dzina la Chauta, ndipo ngati zolankhula zakezo sizichitika, pomwepo dziŵani kuti si mau a Chauta amenewo. Mneneri ameneyo wongolankhula zakezake modzikhulupirira, musamuwope ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati zimene mneneriyo wanenera mʼdzina la Yehova sizinachitike kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti umenewo si uthenga umene Yehova wayankhula. Mneneri ameneyo amangoyankhula za mʼmutu mwake ndiye musadzidzimuke naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sacitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanena; mneneriyo ananena modzikuza, musamuopa iye.